Mlungu dalitsani Malaŵi Mumsunge m'mtendere Gonjetsani adani onse Njala, nthenda, nsanje Lunzitsani mitima yathu Kuti tisaope Mdalitse mtsogoleri nafe Ndi mayi Malaŵi Malaŵi ndziko lokongola La chonde ndi ufulu Nyanja ndi mphepo ya m'mapiri Ndithudi tadala Zigwa, mapiri, nthaka, dzinthu N'mphatso zaulere Nkhalango, madambo abwino Ngwokoma Malaŵi O ufulu tigwirizane Kukweza Malaŵi Ndi chikondi, khama, kumvera Timutumikire Pa nkhondo nkana pa mtendere Cholinga n'chimodzi Mayi, bambo, tidzipereke Pokweza Malaŵi